Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Akolose 3:7 - Buku Lopatulika

zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Inunso kale makhalidwe anu anali omwewo, munkachita zomwezo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Inunso kale munkachita zomwezi, mʼmoyo wanu wakale uja.

Onani mutuwo



Akolose 3:7
7 Mawu Ofanana  

Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za machimo, zimene zinali mwa chilamulo, zinalikuchita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso.


Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera;


Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.