Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumtulutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama?
Akolose 3:6 - Buku Lopatulika chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chifukwa cha zinthu zotere Mulungu amaŵakwiyira anthu osamumvera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa cha zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa ana osamvera. |
Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumtulutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama?
Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m'chosalungama chao;
Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.
okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.