Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
Akolose 3:18 - Buku Lopatulika Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu akazi, gonjerani amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. |
Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
Ndipo mau amene adzaika mfumu akamveka mu ufumu wake wonse, (pakuti ndiwo waukulu), akazi onse adzachitira amuna ao ulemu, aakulu ndi aang'ono.
Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.
Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.
Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;
Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete.