Koma zipatso za mtengo umene uli m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.
Akolose 2:21 - Buku Lopatulika usaikapo dzanja, usalawa, usakhudza, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 usaikapo dzanja, usalawa, usakhudza, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Usagwire chakuti”, “Usakhudze chakuti”? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Usagwire chakuti,” “Usalawe chakuti,” “Usakhudze chakuti?” |
Koma zipatso za mtengo umene uli m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.
Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.
Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,
Ngati munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nazo zoyamba za dziko lapansi, mugonjeranji kuzoikikazo, monga ngati moyo wanu mukhala nao m'dziko lapansi,
a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.