Akolose 1:26 - Buku Lopatulika ndiwo chinsinsicho chinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anachionetsa tsopano kwa oyera mtima ake, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndiwo chinsinsicho chinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anachionetsa tsopano kwa oyera mtima ake, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mauwo ndi chinsinsi chozama chimene chinali chobisika chikhalire kwa mibadwo yonse, koma tsopano Mulungu wachiwululira anthu ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero chinsinsi chimene chakhala chikubisika kwa nthawi ndi mibado, koma tsopano chawululidwa kwa oyera mtima. |
Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.
Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa.
Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zichitidwa m'mafanizo;
Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse.
koma tilankhula nzeru ya Mulungu m'chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu,
kuti itonthozeke mitima yao, nalumikizike pamodzi iwo m'chikondi, kufikira chuma chonse cha chidzalo cha chidziwitso, kuti akazindikire iwo chinsinsi cha Mulungu, ndiye Khristu,
ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,
koma chaonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino,