Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.
Ahebri 9:16 - Buku Lopatulika Pakuti pamene pali chopangiratu pafunika pafike imfa ya wolemberayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti pamene pali chopangiratu pafunika pafike imfa ya wolemberayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati munthu alemba Chipangano chosiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba chipanganocho wamwaliradi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati munthu alemba pangano losiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba panganolo wamwaliradi, |
Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.
Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.
ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,
Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,
Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.
Pakuti chopangiratu chiona mphamvu atafa mwini wake; popeza chilibe mphamvu konse pokhala wolemberayo ali ndi moyo;
Pakuti aliyense amene angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse.