Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo.
Ahebri 8:7 - Buku Lopatulika Pakuti loyamba lija likadakhala lopanda chilema sakadafuna malo a lachiwirilo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti loyamba lija likadakhala lopanda chilema sakadafuna malo a lachiwirilo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chipangano choyamba chija chikadakhala changwiro, sipakadafunikanso china m'malo mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati pangano loyamba lija likanakhala langwiro, sipakanafunikanso lina mʼmalo mwake. |
Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo.
Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?
Pakutitu kuli kutaya kwake kwa lamulo lidadza kalelo, chifukwa cha kufooka kwake, ndi kusapindulitsa kwake,
Koma tsopano Iye walandira chitumikiro chomveka koposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.