chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.
Ahebri 8:4 - Buku Lopatulika Ndipo Iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mitulo monga mwa lamulo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mitulo monga mwa lamulo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyu akadakhala pa dziko lapansi, sibwenzi ali wansembe konse, popeza kuti alipo kale ansembe amene amapereka mphatso potsata Malamulo a Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati iye akanakhala pa dziko lapansi, sakanakhala wansembe pakuti alipo kale anthu amene amapereka mphatso zolembedwa mʼMalamulo. |
chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.
Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israele.
Ndipotu wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawirikawiri, zimene sizingathe konse kuchotsa machimo;
Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.
Pakuti mkulu wa ansembe aliyense, wotengedwa mwa anthu, amaikika chifukwa cha anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe chifukwa cha machimo:
amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira chifukwa cha zoipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoipa za anthu; pakuti ichi anachita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.
Pakuti mkulu wa ansembe aliyense aikidwa kupereka mitulo, ndiponso nsembe; potero nkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka.
ndicho chiphiphiritso cha kunthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbumtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.