Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndili ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.
Ahebri 7:8 - Buku Lopatulika Ndipo pano anthu ofeka alandira limodzi la magawo khumi; koma apo iye, woti adamchitira umboni kuti ali ndi moyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pano anthu ofeka alandira limodzi la magawo khumi; koma apo iye, woti adamchitira umboni kuti ali ndi moyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kunena za ansembe olandira chachikhumi aja, amene ndi zidzukulu za Levi, iwoŵa ndi anthu otha kufa. Koma kunena za Melkizedeki, Malembo amamchitira umboni kuti ngwamoyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ansembe amene amalandira chakhumi amafa, choncho Melikizedeki ndi wamkulu kuwaposa iwo chifukwa Malemba amamuchitira umboni kuti ndi wamoyo. |
Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndili ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adatuluka mu Ejipito ndi Mose?
Monga anenanso mwina, Iwe ndiwe wansembe wa nthawi zonse monga mwa dongosolo la Melkizedeki.
m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.
Ndipo kuli ngati kunena, mwa Abrahamu Levinso wakulandira limodzilimodzi la magawo khumi adapereka limodzi la magawo khumi;
ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.