Yehova walumbira, ndipo sadzasintha, Inu ndinu wansembe kosatha monga mwa chilongosoko cha Melkizedeki.
Ahebri 7:21 - Buku Lopatulika koma Iye ndi lumbiro mwa Iye amene anenana kwa Iye, Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa, iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha). Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma Iye ndi lumbiro mwa Iye amene anenana kwa Iye, Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa, iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha). Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yesu adaloŵa unsembe wake ndi lumbiro, pamene Mulungu adamuuza kuti, “Ambuye adalumbira, ndipo sadzasintha maganizo ake akuti, ndiwe wansembe mpaka muyaya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yesu ankakhala wansembe ndi lumbiro pamene Mulungu anati, “Ambuye analumbira ndipo sangasinthe maganizo ake, ‘Iwe ndi wansembe wamuyaya.’ ” |
Yehova walumbira, ndipo sadzasintha, Inu ndinu wansembe kosatha monga mwa chilongosoko cha Melkizedeki.
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?
Monga anenanso mwina, Iwe ndiwe wansembe wa nthawi zonse monga mwa dongosolo la Melkizedeki.
pakuti amchitira umboni, Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.
Ndipo monga momwe sikudachitike kopanda lumbiro; (pakuti iwotu anayesedwa ansembe kopanda lumbiro;
Pakuti chilamulo chimaika akulu a ansembe anthu, okhala nacho chifooko; koma mau a lumbirolo, amene anafika chitapita chilamulo, aika Mwana, woyesedwa wopanda chilema kunthawi zonse.
Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa.