ndipo mwa Iye yense wokhulupirira ayesedwa wolungama kumchotsera zonse zimene simunangathe kudzichotsera poyesedwa wolungama ndi chilamulo cha Mose.
Ahebri 7:18 - Buku Lopatulika Pakutitu kuli kutaya kwake kwa lamulo lidadza kalelo, chifukwa cha kufooka kwake, ndi kusapindulitsa kwake, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakutitu kuli kutaya kwake kwa lamulo lidadza kalelo, chifukwa cha kufooka kwake, ndi kusapindulitsa kwake, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero lamulo lakale lalekeka chifukwa linali lopanda mphamvu, linali lopanda phindu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho lamulo loyamba lachotsedwa chifukwa linali lofowoka ndi lopanda phindu. |
ndipo mwa Iye yense wokhulupirira ayesedwa wolungama kumchotsera zonse zimene simunangathe kudzichotsera poyesedwa wolungama ndi chilamulo cha Mose.
Potero kodi lamulo tiyesa chabe mwa chikhulupiriro? Msatero ai; koma tikhazikitsa lamulo.
Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;
Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo.
Ndipo ichi ndinena: Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lachabe.
Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo.
koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?
pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.
Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.
(pakuti chilamulo sichinachitire kanthu kakhale kopanda chilema), ndipo kulinso kulowa nacho chiyembekezo choposa, chimene tiyandikira nacho kwa Mulungu.