Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
Ahebri 7:14 - Buku Lopatulika Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhula kanthu ka ansembe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchodziŵikiratu kuti Ambuye athu aja anali a fuko la Yuda, ndipo Mose pokamba za fuko limeneli, sadanenepo kanthu za ansembe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti nʼzodziwika bwino kuti Ambuye athu anachokera fuko la Yuda. Kunena za fuko limeneli, Mose sananenepo kanthu za ansembe. |
Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.
Ndipo padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese, ndi nthambi yotuluka m'mizu yake idzabala zipatso;
Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.
Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraele.
mwana wa Aminadabu, mwana wa Admini, mwana wa Arini, mwana wa Hezironi, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,
Ndipo iwowa ananena kwa iye, Mkazi, uliranji? Ananena nao, Chifukwa anachotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene anamuika Iye.
Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wa Mulungu?
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,
Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.
Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melkizedeki,
Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukuchitirani umboni za izi mu Mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.
ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.