chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.
Ahebri 7:13 - Buku Lopatulika Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ambuye athu, amene mauŵa akunena za Iwo, anali a fuko lina. Ndipo palibiretu wa fuko limeneli amene adatumikirapo ku guwa lansembe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ambuye athu Yesu, amene mawuwa akunena za Iye, anali wa fuko lina, ndipo palibe aliyense wochokera fuko lakelo amene anatumikira pa guwa lansembe. |
chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.
Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israele amene adandaula nao pa inu.
Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?
Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe.