Ahebri 7:12 - Buku Lopatulika Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti pakakhala kusintha pa unsembe, ndiye kuti pa Malamulonso sipangalephere kukhala kusintha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti pamene unsembe usintha, malamulonso amayenera kusintha. |
Pamenepo udzakumbukira njira zako ndi kuchita manyazi, pakulandira abale ako aakulu ndi aang'ono; ndipo ndidzakupatsa awa akhale ana ako aakazi, angakhale sali a pangano lako.
Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?
Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.
Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.