Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Ahebri 7:10 - Buku Lopatulika

pakuti pajapo anali m'chuuno cha atate wake, pamene Melkizedeki anakomana naye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

pakuti pajapo anali m'chuuno cha atate wake, pamene Melkizedeki anakomana naye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pakuti iye anali akadali m'thupi la kholo lake Abrahamu pamene Melkizedeki adadzamchingamira.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

chifukwa pamene Melikizedeki anakumana ndi Abrahamu nʼkuti Levi ali mʼthupi la kholo lake.

Onani mutuwo



Ahebri 7:10
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m'chuuno mwako;


Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo mu Ejipito, amene anatuluka m'chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana aamuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;


Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzatuluka m'chuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba.


Monga anenanso mwina, Iwe ndiwe wansembe wa nthawi zonse monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?


Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira ntchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kwa abale ao, angakhale adatuluka m'chuuno cha Abrahamu;


Ndipo kuli ngati kunena, mwa Abrahamu Levinso wakulandira limodzilimodzi la magawo khumi adapereka limodzi la magawo khumi;