Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Ahebri 5:11 - Buku Lopatulika

Za iye tili nao mau ambiri kuwanena, ndi otivuta powatanthauzira, popeza mwagontha m'makutu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Za iye tili nao mau ambiri kuwanena, ndi otilaka powatanthauzira, popeza mwagontha m'makutu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tili ndi zambiri zoti nkunena pa zimenezi, koma nzovuta kufotokoza kwake, popeza kuti mwasanduka ouma mitu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tili ndi zambiri zoti tinganene pa zimenezi, koma ndi zovuta kukufotokozerani chifukwa ndinu ochedwa kuphunzira.

Onani mutuwo



Ahebri 5:11
12 Mawu Ofanana  

Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa.


Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe.


Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m'makutu ao anamva mogontha, ndipo maso ao anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo.


Ndipo Iye ananena nao, Simudziwitsa ngakhale tsopano kodi?


Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!


Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.


Koma ananena ichi kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha chimene adzachita.


pakuti mtima wa anthu awa watupatu, ndipo m'makutu mwao mmolema kumva, ndipo maso ao anawatseka; kuti angaone ndi maso, nangamve ndi makutu, nangazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo Ine ndingawachiritse.


wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.


monganso m'makalata ake onse pokamba momwemo za izi; m'menemo muli zina zovuta kuzizindikira, zimene anthu osaphunzira ndi osakhazikika apotoza, monganso atero nao malembo ena, ndi kudziononga nao eni.