Ahebri 3:2 - Buku Lopatulika amene anakhala wokhulupirika kwa Iye adamuikayo, monganso Mose m'nyumba yake yonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 amene anakhala wokhulupirika kwa Iye adamuikayo, monganso Mose m'nyumba yake yonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene adampatsa udindowo, monga momwe Mosenso anali wokhulupirika m'nyumba yonse ya Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamupatsa udindowo, monga momwe Mose anali wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu. |
Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.
Ine ndalemekeza Inu padziko lapansi, m'mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.
Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.
Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiye Iye pa ndekha; chifukwa ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse.
Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati padziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu.
Ndimyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,
kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.
Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.
Ndipo Samuele ananena ndi anthuwo, Yehova ndiye amene anaika Mose ndi Aroni, natulutsanso makolo anu m'dziko la Ejipito.