Ahebri 3:11 - Buku Lopatulika Monga ndinalumbira mu ukali wanga: Ngati adzalowa mpumulo wanga! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Monga ndinalumbira m'ukali wanga: Ngati adzalowa mpumulo wanga! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero ndili wokwiya ndidalumbira kuti, ‘Sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Ine ndinalumbira nditakwiya kuti, ‘Iwo sadzalowa mu mpumulo wanga.’ ” |
Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m'chigwamo; tembenukani mawa, nimunke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.
Ine Yehova ndanena, ndidzachitira ndithu ichi khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'chipululu muno, nadzafamo.
Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira.
Popeza ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena, Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Zingakhale ntchitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi.