Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu padziko lapansi, ndipo anavutika m'mtima mwake.
Ahebri 3:10 - Buku Lopatulika Momwemo ndinakwiya nao mbadwo uwu, ndipo ndinati, Nthawi zonse amasochera mumtima; koma sanazindikire njira zanga iwowa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemo ndinakwiya nao mbadwo uwu, ndipo ndinati, Nthawi zonse amasochera mumtima; koma sanazindikira njira zanga iwowa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ndidaukwiyira mbadwowo, ndipo ndidati, ‘Nthaŵi zonse amasokera mumtima mwao, sanaphunzirebe njira zanga.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake ndinawukwiyira mʼbadowo, ndipo Ine ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera, ndipo iwo sadziwa njira zanga.’ |
Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu padziko lapansi, ndipo anavutika m'mtima mwake.
Ndi kuti asange makolo ao, ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; mbadwo wosakonza mtima wao, ndi mzimu wao sunakhazikike ndi Mulungu.
Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga.
Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza.
Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.
Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.
Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.
Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.
Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;
Pakuti ngati choonadi cha Mulungu chichulukitsa ulemerero wake chifukwa cha bodza langa, nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wochimwa?
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.
Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;
Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele.