Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.
Ahebri 2:5 - Buku Lopatulika Pakuti sanagonjetsere angelo dziko lilinkudza limene tinenali. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti sanagonjetsera angelo dziko lilinkudza limene tinenali. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tikamanena za dziko limene lilikudza, si angelo amene Mulungu adaŵapatsa ulamuliro pa dzikolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu sanapereke kwa angelo ulamuliro wa dziko limene likubwerali, limene ife tikulinena. |
Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.
Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m'menemo mukhalitsa chilungamo.
Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.