Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Ahebri 2:12 - Buku Lopatulika Ndi kuti, Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa Mpingo ndidzakuimbirani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi kuti, Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa Mpingo ndidzakuimbirani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ponena mau akuti, “Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu. Ndidzakutamandani pa msonkhano wa anthu anu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye akuti, “Ine ndidzawuza abale anga za dzina lanu. Ndidzakuyimbirani nyimbo zamatamando pamaso pa mpingo.” |
Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.
Chilungamo chanu sindinachibise m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisire msonkhano waukulu.
Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi mu Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhule kanthu.
ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa mu Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro,