Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Ahebri 13:6 - Buku Lopatulika Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero ife tikunena molimba mtima kuti, “Ambuye ndiye mthandizi wanga; sindidzachita mantha. Munthu angandichitenji ine?” |
Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.
Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga.
Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?
Pakuti munakhala mthandizi wanga; ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.
ndi dzina la mnzake ndiye Eliyezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.
Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.
amene tili naye chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye.
Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe, wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza, ndi pa mitambo mu ukulu wake.
Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.
Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
Ndipo iye ananena naye, Usaopa; chifukwa dzanja la Saulo atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israele, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Saulo atate wanga achidziwa.