Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo.
Ahebri 13:11 - Buku Lopatulika Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa, ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, chifukwa cha zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa, ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, chifukwa cha zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mkulu wa ansembe amatenga magazi kukapereka nsembe chifukwa cha machimo, koma nyamayo imawotchedwa kunja kwa msasa. |
Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo.
Utengenso ng'ombe ya nsembe yauchimo, aipsereze pamalo oikika a Kachisi kunja kwa malo opatulika.
Koma ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndi mbuzi ya nsembe yauchimo, zimene mwazi wao analowa nao kuchita nao chotetezera m'malo opatulika, atuluke nazo kunja kwa chigono; natenthe ndi moto zikopa zao, ndi nyama zao, ndi chipwidza chao.
Pamenepo avule zovala zake, navale zovala zina, nachotse phulusa kunka nalo kunja kwa chigono, kumalo koyera.
Koma asadye nsembe yauchimo iliyonse, imene amadza nao mwazi wake ku chihema chokomanako kutetezera nao m'malo opatulika; aitenthe ndi moto.
Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anaviika chala chake m'mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde paguwa la nsembe;
ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake.
Pamenepo wansembe atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi; ndipo atatero alowenso kuchigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.