Uzilandira kwa iwo, kuti zikhale zakuchitira ntchito ya chihema chokomanako; nuzipereke kwa Alevi, yense monga mwa ntchito yake.
Ahebri 13:10 - Buku Lopatulika Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ife tili ndi guwa lansembe, ndipo ansembe otumikira mʼtenti cha Ayuda, saloledwa kudya zochokera pamenepo. |
Uzilandira kwa iwo, kuti zikhale zakuchitira ntchito ya chihema chokomanako; nuzipereke kwa Alevi, yense monga mwa ntchito yake.
Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.
Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za mu Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?
amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.