Ahebri 12:8 - Buku Lopatulika Koma ngati mukhala opanda chilango, chimene onse adalawako, pamenepo muli am'thengo, si ana ai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati mukhala opanda chilango, chimene onse adalawako, pamenepo muli am'thengo, si ana ai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati Mulungu sakulangani inuyo, monga amachitira ndi ana ake onse, ndiye kuti sindinu ana enieni, koma am'chigololo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo. |
Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.