Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;
Ahebri 12:6 - Buku Lopatulika pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda ndipo amalanga aliyense amene amamulandira.” |
Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;
Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova, ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.
Chifukwa chake, mwa ichi choipa cha Yakobo chidzafafanizidwa, ndipo ichi ndi chipatso chonse chakuchotsa tchimo lake; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.
Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.
Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.
Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.