Ahebri 12:12 - Buku Lopatulika Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake limbitsani manja anu otopa ndi mawondo anu ogowoka. |
Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo chifukwa ninji? Uzikati, Chifukwa cha mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uliwonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uliwonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona ilinkudza, inde idzachitika, ati Ambuye Yehova.
Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.
Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.
Pakuti talingirirani Iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m'moyo mwanu.
ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana, Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye, kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye;