Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Ahebri 11:6 - Buku Lopatulika koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa. |
Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.
Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama. Indedi, pali Mulungu wakuweruza padziko lapansi.
Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.
Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.
ndipo mutu wa Efuremu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wa Remaliya, mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika.
Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?
Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Popeza simunandikhulupirira Ine, kundipatula Ine pamaso pa ana a Israele, chifukwa chake simudzalowetsa msonkhano uwu m'dziko ndinawapatsali.
Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu mu Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.
Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alinkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;
Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.
Ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye amene sanamkhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?
Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.
nawerenga tonzo la Khristu chuma choposa zolemera za Aejipito; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphotho.
Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;
Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindule nao mau omvekawo, popeza sanasakanizike ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.
Popeza tsono patsala kuti ena akalowa momwemo, ndi iwo amene Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa iwo kale sanalowemo chifukwa cha kusamvera,
(pakuti chilamulo sichinachitire kanthu kakhale kopanda chilema), ndipo kulinso kulowa nacho chiyembekezo choposa, chimene tiyandikira nacho kwa Mulungu.
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.
Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse;
Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso;
Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.
Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.
Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake.