Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kamvulumvulu, Eliya anachokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa.
Ahebri 11:5 - Buku Lopatulika Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeke, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pokhala ndi chikhulupiriro, Enoki adatengedwa kupita Kumwamba, osafa konse. Sadapezekenso, popeza kuti Mulungu adamtenga. Malembo amamchitira umboni kuti asanatengedwe, anali wokondweretsa Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa wamoyo, motero iye sanalawe imfa; sanapezeke chifukwa Mulungu anamutenga. Pakuti asanatengedwe anayamikiridwa kuti ankakondweretsa Mulungu. |
Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kamvulumvulu, Eliya anachokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa.
Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu.
Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa? Amene adzapulumutsa moyo wake kumphamvu ya manda?
Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.
Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Khristu wake wa Ambuye.
mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Mahalalele, mwana wa Kainani,
komatu monga Mulungu anativomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu aliyense.
ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.
Ndipo kwa iwo, Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira kwa Adamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi,