Ahebri 10:9 - Buku Lopatulika pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzachita chifuniro chanu. Achotsa choyambacho, kuti akaike chachiwiricho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzachita chifuniro chanu. Achotsa choyambacho, kuti akaike chachiwiricho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma pambuyo pake adati, “Ndabweratu, kuti ndichite zimene mukufuna.” Motero Khristu adathetsa mphamvu za nsembe za mtundu woyamba zija, kuti m'malo mwake akhazikitse nsembe ya mtundu wachiŵiriyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri. |
kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.
pamenepo ndinati, Taonani, ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.