Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.
Ahebri 10:8 - Buku Lopatulika Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifune, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo), Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo), Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero poyamba adati, “Nsembe kapena zopereka, nsembe zopsereza kwathunthu kapenanso nsembe zoperekera machimo, simudazifune ndipo simudakondwere nazo.” Zimenezi nzimene Malamulo adaanena kuti ziperekedwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe. |
Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.
ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzake monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.
Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;
Mwa ichi polowa m'dziko lapansi, anena, Nsembe ndi chopereka simunazifune, koma thupi munandikonzera Ine.