ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Ahebri 10:7 - Buku Lopatulika pamenepo ndinati, Taonani, ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pamenepo ndinati, Taonani, ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ine ndidati, ‘Inu Mulungu, ndabweratu kuti ndichite zimene mukufuna, paja zidalembedwa choncho ponena za Ine m'buku la Malamulo.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine, Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’ ” |
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Napeza ku Ekibatana m'nyumba ya mfumu m'dera la Mediya, mpukutu, ndi m'menemo munalembedwa motere, chikhale chikumbutso:
Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhale wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.
Tenga buku lampukutu, nulembe m'menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israele, ndi akunenera Yuda, ndi akunenera amitundu onse kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero.
Ndipo pakupenya ine ndinaona dzanja londitulutsira, ndipo taonani, mpukutu wa buku m'mwemo;
Ndipo ananena nane, Wobadwa ndi munthu iwe, Idya chimene wachipeza; idya mpukutu uwu, numuke ndi kunena ndi nyumba ya Israele.
Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.
Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.
Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.