Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?
Ahebri 10:3 - Buku Lopatulika Komatu mu izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Komatu mu izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma monga zilirimu, nsembezo zimakumbutsa anthu za machimo ao chaka ndi chaka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka. |
Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?
Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.
Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose.
pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.
koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;