Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.
Ahebri 10:2 - Buku Lopatulika Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbumtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbu mtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo. |
Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.
Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.
Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.
Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya.
Iwenso, chifukwa cha mwazi wa pangano lako ndinatulutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.
Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.