Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Ahebri 10:13 - Buku Lopatulika kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando kumapazi ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando kumapazi ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala ngati chopondapo mapazi ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake. |
Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.
Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale padzanja lamanja langa, kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako.
Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.
Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala padzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako?