Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.
Ahebri 1:12 - Buku Lopatulika ndi monga chofunda mudzaipinda monga malaya, ndipo idzasanduka; koma Inu ndinu yemweyo, ndipo zaka zanu sizidzatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi monga chofunda mudzaipinda monga malaya, ndipo idzasanduka; koma Inu ndinu yemweyo, ndipo zaka zanu sizidzatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudzazipindapinda ngati mwinjiro, ndipo zidzasinthika ngati chovala, koma Inu ndinu osasinthika, zaka zanu sizidzatha konse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mudzazipindapinda ngati chofunda; ndipo zidzasinthidwa ngati chovala. Koma Inu simudzasintha, ndipo zaka zanu sizidzatha.” |
Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.
Pakuti pamaso panu zaka zikwi zikhala ngati dzulo, litapita, ndi monga ulonda wa usiku.
Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.
Pokhala panga pachotsedwa, pandisunthikira monga hema wa mbusa; Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba; Iye adzandidula ine poomberapo; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.
Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.