Afilipi 2:20 - Buku Lopatulika Pakuti ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndilibenso wina wonga amene ali ndi mtima wosamala za inu kwenikweni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndilibenso wina monga iyeyu amene ali ndi chidwi chenicheni pa za moyo wanu. |
Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.
Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;
Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;
kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;
Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.
ndi Yesu, wotchedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo antchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.
kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa m'mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;
pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa agogo ako Loisi, ndi mwa mai wako Yunisi, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.
Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro,
Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.
Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha.