Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.
Aefeso 6:4 - Buku Lopatulika Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye. |
Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.
Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Limbika, nulimbe mtima, nuchichite; usaopa, kapena kutenga nkhawa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusowa kapena kukutaya mpaka zitatha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova.
nimupatse Solomoni mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kuchita izi zonse, ndi kumanga chinyumbachi chimene ndakonzeratu mirimo yake.
Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.
Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.
ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.
pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa agogo ako Loisi, ndi mwa mai wako Yunisi, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.
Nati Manowa, Achitike tsopano mau anu; koma makhalidwe ake a mwanayo ndi machitidwe ake adzatani?