Aefeso 5:7 - Buku Lopatulika Chifukwa chake musakhale olandirana nao; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake musakhale olandirana nao; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake musamagwirizane nawo anthu otere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere. |
Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.
Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?
kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino,
Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.
Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;