Aefeso 5:4 - Buku Lopatulika kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiponso musamalankhule zolaula, zopusa, kapena zopandapake, koma muzilankhula zoyamika Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika. |
Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa.
Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.
zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:
koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pamalo pomwe adadyapo mkate m'mene Ambuye Yesu adayamika;
Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;
pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.
Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:
Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu;
Momwemo, ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu mu Khristu kukulamulira chimene chiyenera,
Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.
Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;
Koma iwowa zimene sazidziwa azichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika.
mafunde oopsa a nyanja, akuwinduka thovu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.