Pakuti iwe unachichita m'tseri; koma Ine ndidzachita chinthu ichi pamaso pa Aisraele onse, dzuwa lili nde.
Aefeso 5:12 - Buku Lopatulika pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri. |
Pakuti iwe unachichita m'tseri; koma Ine ndidzachita chinthu ichi pamaso pa Aisraele onse, dzuwa lili nde.
Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.
Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.
tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.
Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika.
Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;
Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;
Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao.