Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
Aefeso 5:10 - Buku Lopatulika kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye. |
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
Kodi kusala kudya koteroko ndiko ndinakusankha? Tsiku lakuvutitsa munthu moyo wake? Kodi ndiko kuweramitsa mutu wake monga bango, ndi kuyala chiguduli ndi phulusa pansi pake? Kodi uyesa kumeneko kusala kudya, ndi tsiku lovomerezeka kwa Yehova?
Lubani andifumiranji ku Sheba, ndi nzimbe ku dziko lakutali? Nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.
Pakuti iye amene atumikira Khristu mu izi akondweretsa Mulungu, navomerezeka ndi anthu.
kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Khristu;
Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.
kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;
Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.
Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.
Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu.
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.
Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesere kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindingathe kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowere. Nazivula Davide.