Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye.
Aefeso 4:7 - Buku Lopatulika Ndipo kwa yense wa ife chapatsika chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Khristu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kwa yense wa ife chapatsika chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Khristu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe aliyense wa ife adalandira mphatso yakeyake yaulere, molingana ndi m'mene Khristu amaperekera mphatso zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma aliyense wa ife wapatsidwa chisomo molingana ndi muyeso wa mphatso ya Khristu. |
Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye.
Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso.
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.
Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,
Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;
pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;