Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?
Aefeso 4:27 - Buku Lopatulika ndiponso musampatse malo mdierekezi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndiponso musampatse malo mdierekezi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musampatse mpata Satana woti akugwetseni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musamupatse mpata Satana. |
Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?
Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.
Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.
koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: