Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'chifanizo cha Mulungu;
Aefeso 4:24 - Buku Lopatulika nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero. |
Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'chifanizo cha Mulungu;
Ndinavala chilungamo, ndipo chinandivala ine; chiweruzo changa chinanga mwinjiro ndi nduwira.
Galamuka! Galamuka! Tavala mphamvu zako, Ziyoni; tavala zovala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa.
Ndipo anavala chilungamo monga chida chapachifuwa, ndi chisoti cha chipulumutso pamutu pake; navala zovala zakubwezera chilango, navekedwa ndi changu monga chofunda.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika.
Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.
Koma tsopano tinamasulidwa kuchilamulo, popeza tinafa kwa ichi chimene tinagwidwa nacho kale; chotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m'chilembo chakale ai.
Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;
Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.
Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.
Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano.
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
atachotsa udani m'thupi lake, ndiwo mau a chilamulo cha kutchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kuchitapo mtendere;
Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.
Koma ponena za Mwana, ati, Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi; ndipo ndodo yachifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;
mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili padziko lapansi m'chilakolako.