Aefeso 3:13 - Buku Lopatulika Mwa ichi ndipempha kuti musade mtima m'zisautso zanga chifukwa cha inu, ndiwo ulemerero wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwa ichi ndipempha kuti musade mtima m'zisautso zanga chifukwa cha inu, ndiwo ulemerero wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikukupemphani tsono kuti musataye mtima chifukwa chakuti ndikukusaukirani. Kwenikweni muyenera kunyadira chifukwa cha kusauka kwangaku. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho, ine ndikukupemphani kuti musakhumudwe popeza ndikusautsidwa chifukwa cha inu pakuti masautso angawa ndi ulemerero wanu. |
nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.
Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.
nati nao, Tamverani, Israele, muyandikiza kunkhondo lero pa adani anu; musafumuka mitima yanu; musachita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao;
Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;