Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.
Aefeso 3:10 - Buku Lopatulika kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsopano afuna kuti kudzera mwa Mpingo, mafumu ndi aulamuliro onse a Kumwamba adziŵe nzeru za Mulungu zamitundumitundu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Cholinga chake tsopano nʼchakuti, kudzera mwa mpingo, mafumu ndi a ulamuliro onse a kumwamba adziwe nzeru zochuluka za Mulungu. |
Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.
Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.
Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukulu, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m'malo mwake.
Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu,
koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.
koma tilankhula nzeru ya Mulungu m'chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu,
pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m'nyengo ino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza;
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.
pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye.
Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.
Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.
amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.