Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveke kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena chipangizo chachitsulo, pomangidwa iyo.
Aefeso 2:21 - Buku Lopatulika mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwa Iyeyo, nyumba yonse yalumikizidwa pamodzi ndipo yakwezedwa kukhala Nyumba yoyera mwa Ambuye. |
Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveke kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena chipangizo chachitsulo, pomangidwa iyo.
Mboni zanu zivomerezeka ndithu; chiyero chiyenera nyumba yanu, Yehova, kunthawi za muyaya.
Ndi monga mwa makomo a zipinda za kumwera panali khomo polekeza njira, ndiyo njira yokhudzana ndi linga la kum'mawa polowamo.
Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.
Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.
kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.
kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.