ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Aefeso 1:22 - Buku Lopatulika ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamutu pa zonse, kwa Mpingo Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa Mpingo Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adagonjetsa zonse kuti zikhale pansi pa mapazi a Khristu, ndipo adamkhazika pamwamba pa zonse kuti akhale mutu wa Mpingo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo, |
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.
Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.
Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.
kwa Iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.
Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.
Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.
kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.
kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.
mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Pakuti muja adagonjetsa zonse kwa iye, sanasiyepo kanthu kosamgonjera iye. Koma sitinayambe tsopano apa kuona zonse zimgonjera.