Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu:
Aefeso 1:16 - Buku Lopatulika sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu m'mapemphero anga; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu m'mapemphero anga; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake sindilekeza kuthokoza Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani m'mapemphero anga, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga. |
Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu:
Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete,
Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu,
Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kukumbukira inu m'mapemphero athu;
Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;
Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.
Ndipo ana a Israele anati kwa Samuele, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti Iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo.